Proverbs 18

1Munthu wokonda kukhala yekha amafunafuna zomukomera yekha;
iye amatsutsana ndi malangizo onse anzeru.

2Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu,
koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.

3Kuyipa mtima kukabwera, manyozonso amabwera.
Manyazi amabwera pamodzi ndi kunyozeka.

4Mawu a munthu ali ngati madzi akuya,
kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wotumphuka.

5Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu;
kapena kupondereza munthu wosalakwa.

6Mawu a chitsiru amautsa mkangano;
pakamwa pake pamayitana mkwapulo.

7Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake,
ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.

8Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma;
amalowa mʼmimba mwa munthu.

9Munthu waulesi pa ntchito yake
ali pachibale ndi munthu amene amawononga zinthu.

10Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba;
wolungama amathawiramo napulumuka.

11Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba;
chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza.

12Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada,
koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.

13Ukayankha usanamvetse bwino nkhani,
umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.

14Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda,
koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.

15Munthu wanzeru amawonjezera nzeru zina;
amafunafuna kudziwa bwino zinthu.

16Mphatso ya munthu imamutsekulira njira
yomufikitsa pamaso pa anthu akuluakulu.

17Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wolungama ndiye
mpaka mnzake atabwera ndi kumufunsa bwino.

18Kuchita maere kumathetsa mikangano;
amalekanitsa okangana amphamvu.

19Mʼbale amene wamuthandiza amakhala ngati mzinda wolimba,
koma kukangana naye kumatsekereza thandizo.

20Munthu amapeza bwino malingana ndi zoyankhula zake.
Adzakhuta ndi zipatso za pakamwa pake.

21Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo.
Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.

22Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino
ndipo Yehova amamukomera mtima.

23Munthu wosauka amapempha
koma munthu wolemera amayankha mwaukali.

24Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso,
koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.
Copyright information for NyaCCL